2 AKORINTO 1 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 Akol. 1.1-3 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya monse:

2Aef. 1.2-3Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chiyamiko pa matonthozo a Mulungu

3Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,

4wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

5Akol. 1.24Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.

6Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.

7Aro. 8.17Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.

8Mac. 19.23Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;

9Yer. 17.5, 7koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;

10amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;

11Aro. 15.30pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.

Chifukwa cha kuchedwa Paulo kudza ku Korinto

12 2Ako. 2.17 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.

13Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga, kapenanso muvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti mudzavomereza kufikira chimaliziro;

14monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.

15 1Ako. 4.19 Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nacho chisomo chachiwiri;

161Ako. 16.5-6ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.

172Ako. 10.2Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?

18Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhala eya ndi iai.

19Mrk. 1.1Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.

20Aro. 15.8-9Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

211Yoh. 2.20Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;

22Aef. 1.13-14amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

23 Aro. 1.9; 1Ako. 4.21 Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.

24Aro. 15.30; 1Ako. 3.5Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help