1Ndipo iwe, takwezera akalonga a Israele nyimbo ya maliro,
2uziti, Mai wako ndi chiyani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ake pakati pa misona.
32Maf. 23.30-34Ndipo unalera mmodzi wa ana ake, iye nasanduka msona, unaphunzira kugwira nyama, unalusira anthu.
4Mitundu ya anthu idamva mbiri yake, unagwidwa m'mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera kudziko la Ejipito.
5Pakuona tsono waukaziwo, kuti unalindirira, ndi kuti chiyembekezo chake chidatha, unatenga wina wa ana ake, numsandutsa msona.
6Yer. 22.13-18Ndipo unayendayenda pakati pa mikango, nukhala msona, nuphunzira kugwira nyama, nulusira anthu.
7Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula midzi yao, ndipo dziko ndi kudzala kwake linasanduka labwinja, chifukwa cha phokoso la kubangula kwake.
8Pamenepo mitundu ya anthu inadzipereka kuukola kuchokera kumaiko a kumbali zonse, niuphimba ndi ukonde wao, nugwidwa uwu m'mbuna mwao.
92Mbi. 36.6Nauika m'chitatanga ndi zokowera, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni; anaulonga m'malinga, kuti mau ake asamvekenso pa mapiri a Israele.
10 Ezk. 17.6 Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri.
11Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zachifumu, za ochita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, nizinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zake zambiri.
12Ezk. 17.10Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha.
13Ndipo tsopano waokedwa m'chipululu m'dziko louma ndi la ludzu.
142Maf. 24.20Unatulukanso moto kundodo za kunthambi zake, unatha zipatso zake; m'mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yachifumu ya kuchita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.