1 2Maf. 25.1-2 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara.
2Yer. 33.1Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.
3Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,
4ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;
5Yer. 33.5ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?
6Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
7Rut. 4.4Taonani, Hanamele mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.
8Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.
9Gen. 23.16; Mat. 26.15Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.
10Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.
11Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wovundukuka;
12ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.
13Ndipo ndinauza Baruki pamaso pao, kuti,
14Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero; Tenga akalata awa, kalata uyu wogulira, wosindikizidwa, ndi kalata uyu wovundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.
15Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yamphesa idzagulidwanso m'dziko muno.
Pemphero la Yeremiya16Ndipo nditapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti,
17Gen. 18.14; Mat. 19.26Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;
18Yes. 9.6; Eks. 20.6amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu;
19Mas. 62.12; Miy. 5.21; Yes. 28.29wamkulu m'upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;
20Eks. 9.16amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, m'Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;
21Eks. 14.29-31ndipo munatulutsa anthu anu Israele m'dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;
22Eks. 3.8ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uchi;
23Neh. 9.26ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;
24Yer. 32.3taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha chaola; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.
25Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Ababiloni.
Mulungu anenetsa kuti Aisraele adzalangidwa, nalonjeza kuwalanditsanso26Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,
27Yer. 32.17Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine?
28 Yer. 32.3 Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la Ababiloni, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzaulanda,
29Yer. 19.13; 52.13ndipo Ababiloni, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.
30Ezk. 20.28Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.
31Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;
32Dan. 9.8chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu.
33Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.
34Ezk. 8.5-6Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.
35Yer. 7.31Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinauza, chimene sichinalowa m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.
36Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola:
37Yer. 31.10Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,
38Yer. 31.33ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;
39Ezk. 11.19-20ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
40Yes. 55.3ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.
41Deut. 30.9Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
42Yer. 31.28Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa choipa chonsechi, chomwecho ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonjeza.
43Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Ababiloni.
44Yer. 33.7, 11, 26Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kuchidikha, ndi m'midzi ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.