1 AKORINTO 4 - Buku Lopatulika Bible 2014

Atumiki a Khristu ndi ogawira zinsinsi za Mulungu

1 Mat. 24.45 Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.

2Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

3Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.

4Mas. 143.2Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.

5Mat. 7.1; 1Ako. 3.13Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Kudzikuza kwa Akorinto, kudzichepetsa kwa Atumwi

6 Aro. 12.3; 1Ako. 1.12 Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.

7Yoh. 3.27Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?

8Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.

9Aheb. 10.33Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.

10Mac. 26.24; 2Ako. 13.9Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.

112Ako. 11.23-27Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;

12Mac. 20.34ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

13ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.

14Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa.

15Mac. 18.1, 11; Agal. 4.19Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.

16Afi. 3.17Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

171Tim. 1.2Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo m'Mipingo yonse.

18Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.

19Aro. 15.32; 1Ako. 16.5; 2Ako. 1.15, 23; Yak. 4.5Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.

20Pakuti ufumu wa Mulungu suli m'mau, koma mumphamvu. Mufuna chiyani?

212Ako. 2.1-2; 10.2; 13.10Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help