1 MBIRI 4 - Buku Lopatulika Bible 2014

Adzukulu a Yuda

1Ana a Yuda: Perezi, Hezironi, ndi Karimi, ndi Huri, ndi Sobala.

2Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.

3Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezireele, ndi Isima, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi,

4ndi Penuwele atate wa Gedori, ndi Ezere atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efurata atate wa Betelehemu.

5Ndipo Asiriya atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara.

6Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Hefere, ndi Temeni, ndi Haahasitari. Iwo ndiwo ana a Naara.

7Ndi ana a Hela ndiwo Zereti, Izihara, ndi Etinani.

8Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahariyele mwana wa Harumu.

9Gen. 34.19Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ake; ndi make anamutcha dzina lake Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.

10Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.

11Ndipo Kelubu mbale wa Suha anabala Mehiri, ndiye atate wa Esitoni.

12Ndi Esitoni, anabala Beterafa, ndi Paseya, ndi Tehina atate wa Irinahasi. Awa ndi anthu a Reka.

13Yos. 15.17Ndi ana a Kenazi: Otiniyele, ndi Seraya; ndi mwana wa Otiniyele: Hatati.

14Ndipo Meonotai anabala Ofura; ndi Seraya anabala Yowabu atate wa Geharasimu; popeza iwo ndiwo amisiri.

15Num. 13.6Ndi ana a Kalebe mwana wa Yefune: Iru, Ela, ndi Naamu; ndi ana a Ela, ndi Kenazi.

16Ndi ana a Yehalelele: Zifi, ndi Zifa, Tiriya, ndi Asarele.

17Ndi ana a Ezara: Yetere, ndi Meredi, ndi Efere, ndi Yaloni; ndipo anabala Miriyamu, ndi Samai, ndi Isiba atate wa Esitemowa.

18Ndi mkazi wake Myuda anabala Yeredi atate wa Gedori, ndi Hebere atate wa Soko, ndi Yekutiyele atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.

19Ndi ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, ndiwo atate a Keila Mgarimi ndi Esitemowa Mmaaka.

20Ndi ana a Simoni; Aminoni, ndi Rina, Benihanani, ndi Tiloni. Ndi ana a Isi: Zoheti, ndi Benizoheti.

21Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,

22ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yowasi, ndi Sarafi wolamulira m'Mowabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.

23Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala m'Netaimu, ndi m'Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m'ntchito yake.

Adzukulu a Simeoni

24 Gen. 46.10 Ana a Simeoni: Nemuwele, ndi Yamini, Yaribu, Zera, Shaulo,

25Salumu mwana wake, Mibisamu mwana wake, Misima mwana wake.

26Ndi ana a Misima: Hamuele mwana wake, Zakuri mwana wake, Simei mwana wake.

27Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ake analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinachulukitsa ngati ana a Yuda.

28Yos. 19.2Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazara-Suwala,

29ndi ku Biliha, ndi ku Ezemu, ndi ku Toladi,

30ndi ku Betuele, ndi ku Horoma, ndi ku Zikilagi,

31ndi ku Betemara-Kaboti, ndi ku Hazara-Susimu, ndi ku Betebiri, ndi ku Saaraimu. Iyi ndi midzi yao, mpaka ufumu wa Davide, pamodzi ndi milaga yao.

32Etamu, ndi Aini, Rimoni, ndi Tokeni, ndi Asani, midzi isanu;

33ndi milaga yao yonse pozungulira pake pa midzi yomweyi, mpaka Baala. Apo ndi pokhala pao ndipo ali nao mawerengedwe a maina ao.

34Ndi Mesobabu, ndi Yamuleki, ndi Yosa mwana wa Amaziya,

35ndi Yowele, ndi Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asiyele;

36ndi Eliyoenai, ndi Yaakoba, ndi Yesohaya, ndi Asaya, ndi Adiyele, ndi Yesimiele, ndi Benaya,

37ndi Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya;

38awa otchedwa maina ndiwo akalonga m'mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao zinachuluka kwambiri.

39Ndipo anamuka mpaka polowera ku Gedori kum'mawa kwa chigwa, kufunafuna podyetsa zoweta zao.

40Ndipo anapeza podyetsa ponenepetsa ndi pabwino, ndipo dzikoli ndi lachitando ndi lodikha ndi losungikamo, pakuti okhalako kale ndiwo a Hamu.

412Maf. 18.8Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.

42Ndipo ena a iwowa a ana a Simeoni, amuna mazana asanu, ananka kuphiri la Seiri; akuwatsogolera ndiwo Pelatiya, ndi Neariya, ndi Refaya, ndi Uziyele; ana a Isi.

431Sam. 15.8Nakantha otsala a Aamaleke adapulumukawo, nakhala komweko mpaka lero lino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help