1 Eks. 27.1-2 Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi.
21Maf. 7.23-50Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.
3Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.
4Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwera, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi nkholo zao zinayang'anana.
5Ndi kuchindikira kwake kunanga chikhato, ndi mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu.
6Eks. 25.31-40Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.
7Ndipo anapanga zoikapo nyali khumi zagolide, monga mwa ziweruzo chake; naziika m'Kachisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.
8Anapanganso magome khumi, nawaika m'Kachisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolide.
9Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikulu, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zake ndi mkuwa.
10Ndipo anaika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa chakumwera.
11Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake. Natsiriza Huramu ntchito adaichitira mfumu Solomoni m'nyumba ya Mulungu:
12nsanamira ziwiri, ndi zikhozo, ndi mitu iwiri inali pamwamba pa nsanamirazo, ndi maukonde awiri akukuta zikho ziwiri za mitu ili pamwamba pa nsanamirazo,
13ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwa; mizere iwiri ya makangaza ya ukonde uliwonse, akukuta zikho ziwiri za mitu, inali pa nsanamirazo.
14Anapanganso maphaka, napanga mbiya zaphwamphwa khumi pamwamba pa maphaka;
15thawale limodzi ndi ng'ombe khumi ndi ziwiri pansi pake.
16Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zake zonse, Huramuabi anazipangira mfumu Solomoni, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.
17Mfumuyi inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.
18Ndipo Solomoni anazipanga zipangizo izi zonse zochulukadi, pakuti kulemera kwake kwa mkuwa sikunayeseka.
19Solomoni anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolide lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;
20ndi zoikapo nyali ndi nyali zake za golide woona, zakuunikira monga mwa chilangizo chake chakuno cha chipinda chamkati;
21Eks. 25.31-39ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolide, ndiwo golide wangwiro;
22ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zake za m'katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.