1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2Lev. 11.44; 20.7, 26; 1Pet. 1.16Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.
3Eks. 20.12Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
4Eks. 34.17Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
5Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.
6Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwake muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lachitatu, muzikatentha ndi moto.
7Akakadya konse tsiku lachitatu kali chonyansa, kosavomerezeka:
8koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
9 Deut. 24.19; Rut. 2.15, 16 Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.
10Usamakunkha khunkha la m'munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11Eks. 20.15; Akol. 3.9; Aef. 4.25Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana.
12Eks. 20.7; Deut. 5.11Musamalumbira monama ndi kutchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
131Ate. 4.6Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.
14Usamatemberera wogontha; usamaika chokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
15Miy. 24.23Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.
16Mas. 15.3; Miy. 11.13Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.
17Mat. 18.15; Luk. 17.3; 1Yoh. 2.9, 11; 3.15Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.
18Luk. 6.27; Aro. 12.19; Agal. 5.14Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.
19Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana.
20Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.
21Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, ndiyo nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopalamula.
22Ndipo wansembe achite chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula pamaso pa Yehova, chifukwa cha kuchimwa adachimwaku; ndipo adzakhululukidwa chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwaku.
23Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzala mitengo ya mitundumitundu ikhale ya chakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa.
24Koma chaka chachinai zipatso zake zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova.
25Chaka chachisanu muzidya zipatso zake, kuti zobala zake zikuchulukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
26Musamadya kanthu ndi mwazi wake; musamachita nyanga, kapena kuombeza ula.
27Musamameta mduliro, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zanu.
28Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; Ine ndine Yehova.
29Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumchititsa chigololo; lingadzale ndi chigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zochititsa manyazi.
30Mlal. 5.1Muzisunga masabata anga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.
311Sam. 28.7Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
321Tim. 5.1Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
33Eks. 22.21; Mat. 25.35Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa.
34Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
35Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wake, kulemera kwake, kapena kuchuluka kwake.
36Miy. 11.1; 16.11Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.
37Ndipo musamalire malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.