NUMERI 23 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 Num. 23.14 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

2Ndipo Balaki anachita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka pa guwa la nsembe lililonse ng'ombe ndi nkhosa yamphongo.

3Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.

4Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse.

5Yer. 1.9Ndipo Yehova anaika mau m'kamwa mwa Balamu, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.

6Ndipo anabwerera kwa iye, ndipo, taonani, analikuima pa nsembe yopsereza yake, iye ndi akalonga onse a Mowabu.

7Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Ku Aramu ananditenga Balaki,

mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa,

Idza, udzanditembererere Yakobo.

Idza, nudzanyoze Israele.

8Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberere?

Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoze?

9 Eks. 33.16; Deut. 33.28 Pakuti, pokhala pamwamba pa matanthwe ndimpenya,

pokhala pa zitunda ndimuyang'ana;

taonani, ndiwo anthu akukhala pa okha.

Osadziwerengera pakati pa amitundu ena.

10 Gen. 13.16; Mas. 37.37 Adzawerenga ndani fumbi la Yakobo,

kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israele?

Ndipo ine ndife monga amafa oongoka mtima,

chitsiriziro changa chifanane nacho chake!

11Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandichitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu.

12Num. 22.38Ndipo anayankha nati, Chimene achiika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ichi?

13Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.

14Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse.

15Ndipo anati kwa Balaki, Imani pano pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine ndikakomane ndi Iye uko.

16Lev. 23.5Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwake, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.

17Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?

18Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Ukani, Balaki, imvani;

ndimvereni, mwana wa Zipori.

19 1Sam. 15.29; Mala. 3.6; Aro. 11.29; Aheb. 6.18; Tit. 1.2; Yak. 1.17 Mulungu sindiye munthu, kuti aname;

kapena mwana wa munthu, kuti aleke;

kodi anena, osachita?

20 Gen. 12.2 Kapena kulankhula, osachitsimikiza?

Taonani, ndalandira mau akudalitsa,

popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha.

21Sayang'anira mphulupulu ili m'Yakobo,

kapena sapenya kupulukira kuli m'Israele.

Yehova Mulungu wake ali ndi iye,

ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.

22Mulungu awatulutsa m'Ejipito;

mphamvu yake ikunga ya njati.

23 Mas. 44.1 Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo,

kapena ula mwa Israele;

pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele,

chimene Mulungu achita.

24Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi,

nadzitukumula ngati mkango waumuna.

Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira,

utamwa mwazi wa zophedwa.

25Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Usawatemberera konse, kapena kuwadalitsa konse.

26Num. 23.12Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?

27Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.

28Ndipo Balaki ananka naye Balamu pamwamba pa Peori, popenyana ndi chipululu.

29Num. 23.14Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.

30Ndipo Balaki anachita monga adanena Balamu, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help