1 Zek. 9.14 Katundu wa chipululu cha kunyanja. Monga akamvulumvulu a kumwera apitirira, kufumira kuchipululu kudziko loopsa.
2Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.
3Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.
4Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.
5Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta chikopa.
6Pakuti Ambuye atero kwa ine, Muka, ika mlonda anene chimene achiona;
7ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiriawiri, khamu la abulu, khamu la ngamira, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa.
8Ndipo iye anafuulitsa ngati mkango, Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse;
9Yer. 51.8; Chiv. 14.8ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.
10Yer. 51.33Kuomba kwanga nanga, ndi za pa dwale langa: chimene ine ndinachimva kwa Yehova wa makamu Mulungu wa Israele, ndanena kwa inu.
Aneneratu za kuonongeka kwa Duma11Katundu wa Duma. Wina aitana kwa ine kuchokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku?
12Mlonda anati, Kuli kucha, koma kukali usiku; mukafuna kufunsa, funsani, bwerani, idzani.
Za kuonongeka kwa Arabiya13Katundu wa pa Arabiya. M'nkhalango ya m'Arabiya mudzagona, inu makamu oyendayenda a Dedani.
14Muchingamire akumva ludzu ndi madzi; okhala m'dziko la Tema ananka kukomana ndi othawa ndi chakudya chao.
15Pakuti iwo anathawa malupanga, malupanga osololedwa, ndi mauta olifuka ndi nkhondo yovuta.
16Pakuti Ambuye anatero kwa ine, Chisanapite chaka malinga ndi zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wonse wa Kedara udzagoma;
17Yes. 60.7ndi otsala amauta, ngwazi za ana a Kedara zidzachepa, pakuti Yehova Mulungu wa Israele wanena.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.