1Koma Yobu anayankha, nati,
2Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu.
Kulipulumutsa dzanja losalimba!
3Wampangira bwanji wopanda nzeruyu!
Ndi kudziwitsa nzeru zenizeni mochuluka!
4Wafotokozera yani mau?
Ndi mzimu wa yani unatuluka mwa iwe?
5Adafawo anjenjemera
pansi pa madzi ndi zokhalamo.
6 Mas. 139.8, 11; Aheb. 4.13 Kumanda kuli padagu pamaso pake,
ndi kuchionongeko kusowa chophimbako.
7Ayala kumpoto popanda kanthu,
nalenjeka dziko pachabe.
8 Miy. 30.4 Amanga madzi m'mitambo yake yochindikira;
ndi mtambo sung'ambika pansi pake.
9Atchingira pa mpando wake wachifumu,
nayalapo mtambo wake.
10Analembera madziwo malire,
mpaka polekeza kuunika ndi mdima.
11Mizati ya thambo injenjemera,
ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
12 Eks. 14.21 Mwa mphamvu yake agwetsa nyanja bata;
ndipo mwa luntha lake akantha kudzikuza kwake.
13 Mas. 33.6 Mwa mzimu wake anyezimiritsa thambo;
dzanja lake linapyoza njoka yothawayo.
14Taonani, awa ndi malekezero a njira zake;
ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono;
koma kugunda kwa mphamvu yake akudzindikiritsa ndani?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.