1 Miy. 8.13; 16.6; Ezk. 1.14; Yak. 5.11 Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
2Ndipo anabala ana amuna asanu ndi awiri, ndi ana akazi atatu.
3Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu akazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.
4Ndipo ana ake amuna anamuka kukachita madyerero m'nyumba ya yense pa tsiku lake; natumiza mthenga kuitana alongo ao atatu adzadye nadzamwe nao.
51Sam. 16.5Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.
6 Chiv. 12.9-10 Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pao.
7Yob. 2.2; Mat. 12.43; 1Pet. 5.8Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo.
8Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
9Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe?
10Mas. 34.7; 128.1-2Kodi simunamtchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.
11Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.
12Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.
13Tsono panali tsiku loti ana ake aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkulu wao;
14nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng'ombe zinalikulima, ndi abulu akazi analikudya pambali pao;
15koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
16Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
17Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Ababiloni anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamira, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
18Akali chilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkulu wao;
19ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
20 1Pet. 5.6 Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,
21Mas. 49.17; Mlal. 5.19; Mat. 20.15; 1Tim. 6.7; Yak. 1.17nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.
22Yob. 2.10; Mas. 74.22Mwa ichi chonse Yobu sanachimwe, kapena kunenera Mulungu cholakwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.