1 2Sam. 10.1-19 Ndipo zitatha izi, Nahasi mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
2Ndipo Davide anati, Ndidzamchitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wake anandichitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wake. Pofika anyamata ake a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,
3akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kuchitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? Sakudzerani kodi anyamata ake kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?
4Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka achoke.
5Pamenepo anamuka ena namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anachita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndevu zanu; zitamera mubwere.
6Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente chikwi chimodzi a siliva, kudzilembera magaleta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-Maaka, ndi ku Zoba.
7Momwemo anadzilembera magaleta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ake; nadza iwo, namanga misasa chakuno cha Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.
8Pamene Davide anamva ichi anatuma Yowabu ndi gulu lonse la anthu amphamvu.
9Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo ku chipata cha mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo.
10Pakuona Yowabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israele, nawanika ayambane ndi Aaramu.
11Ndipo anthu otsala anawapereka m'dzanja la Abisai mbale wake; ndipo anadzinika ayambane ndi ana a Amoni.
12Ndipo anati, Akandiposa mphamvu Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakuposa mphamvu ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.
13Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi midzi ya Mulungu wathu; ndipo Yehova achite chomkomera.
14Pamenepo Yowabu ndi anthu anali naye anayandikira pamaso pa Aaramu kulimbana nao, ndipo anawathawa.
15Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wake, nalowa m'mudzi. Pamenepo Yowabu anadza ku Yerusalemu.
16Ndipo pakuona Aaramu kuti Israele anawakantha, anatumiza mithenga, natuluka nao Aaramu akukhala tsidya lija la mtsinjewo; ndi Sofaki kazembe wa khamu la Hadadezere anawatsogolera.
17Ndipo anamuuza Davide; namemeza iye Aisraele onse, naoloka Yordani, nawadzera, nanika nkhondo ayambane nao. Atandandalitsa nkhondo Davide kuyambana ndi Aaramu, anaponyana naye.
18Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; ndipo Davide anapha Aaramu apamagaleta zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi anai; napha Sofaki kazembe wa khamulo.
19Ndipo pakuona anyamata a Hadadezere kuti Israele anawakantha, anapangana mtendere ndi Davide, namtumikira; ndi Aaramu anakana kuthandizanso ana a Amoni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.