1 Yes. 40.22 Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu;
ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.
2Usana ndi usana uchulukitsa mau,
ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.
3Palibe chilankhulidwe, palibe mau;
liu lao silimveka.
4Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi,
ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu.
Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,
5ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m'chipinda mwake,
likondwera ngati chiphona kuthamanga m'njira.
6Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo,
ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake;
ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.
7 Mas. 111.7; Aro. 7.12 Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;
mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.
8Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima;
malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
9Kuopa Yehova kuli mbee, kwakukhalabe nthawi zonse;
maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.
10 Mas. 119.72, 127; Miy. 8.10-11, 19 Ndizo zifunika koposa golide,
inde, golide wambiri woyengetsa;
zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.
11 Miy. 29.18 Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo,
m'kuzisunga izo muli mphotho yaikulu.
12 Mas. 90.8 Adziwitsa zolowereza zake ndani?
Mundimasule kwa zolakwa zobisika.
13Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;
zisachite ufumu pa ine.
Pamenepo ndidzakhala wangwiro,
ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.
14 Mas. 51.15; Yes. 43.14; 1Ate. 1.10 Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga
avomerezeke pamaso panu,
Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.