ESTERE Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau OyambaBukuli likukamba za Estere, mtsikana wina wachiyuda, amene ankakonda kwambiri anthu a mtundu wake, naonetsa kulimba mtima kwake pothandiza kuwapulumutsa Ayudawo kwa adani ao. Lifotokozanso za chiyambi chake komanso tanthauzo la chikondwerero cha Chiyuda chotchedwa Purimu.Za mkatimuEstere asankhidwa kuti akhale mfumukazi kudziko la Persiya 1.1—2.23 Hamani apanga chiwembu chifuna kuwonongeratu fuko la Ayuda 3.1—5.14Hamani atsutsidwa naphedwa 6.1—7.10Ayuda agonjetsa adani ao 8.1—10.3