1
26 Aef. 5.12 Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe:
27ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.
28Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
29anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
30akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
31opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;
32Aro. 6.21amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.