1Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.
2Mac. 21.20Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
3Aro. 9.31Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja ku chilungamo cha Mulungu.
4Agal. 3.24Pakuti Khristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa amene aliyense akhulupirira.
5Lev. 18.5Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m'lamulo, adzakhala nacho ndi moyo.
6 Deut. 30.12-13 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chitero, Usamanena mumtima mwako, Adzakwera ndani Kumwambako? Ndiko, kutsitsako Khristu;
7kapena, Adzatsikira ndani ku chiphompho chakuya? Ndiko, kukweza Khristu kwa akufa,
8Deut. 30.14Koma chitani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a chikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:
9Mat. 10.32kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:
10pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m'kamwa avomereza kutengapo chipulumutso.
11Yer. 17.7; Aro. 9.33Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi.
12Mac. 15.9Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye;
13Yow. 2.32; Mac. 2.21pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.
14Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?
15Yes. 52.7; Nah. 1.15Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.
16 Yes. 53.1 Koma sanamvera Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife?
17Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Khristu.
18Mas. 19.4; Akol. 1.23Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu,
Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi,
ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.
19 Deut. 32.21 Koma nditi, Kodi Israele alibe kudziwa? Poyamba Mose anena,
Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi iwo
amene sakhala mtundu wa anthu,
ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.
20 Yes. 65.1 Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati,
Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifuna;
ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunsa.
21 Yes. 65.2 Koma kwa Israele anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.