2 YOHANE Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau Oyamba Kalata yachiwiri yolembedwa ndi mtumwi Yohane inalembedwa ndi “Mkuluyo” kupita kwa “mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake”, amene mwina akutanthauza mpingo ndi anthu ake. Uthenga wake ndi waufupi ndipo ndi wolimbitsana za kukondana komanso kuchenjeza za aphunzitsi onyenga ndi ziphunzitso zawo zachinyengo.Za mkatimuMau oyamba 1.1-3Kufunikira kwa chikondi 1.4-6Awachenjeze asatsate ziphunzitso zonyenga 1.7-11Mau omaliza 1.12-13