MASALIMO 76 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ulemerero ndi mphamvu ya MulunguKwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Salimo la Asafu. Nyimbo.

1Mulungu adziwika mwa Yuda,

dzina lake limveka mwa Israele.

2

3 Ezk. 39.9 Pomwepo anathyola mivi ya pauta;

chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.

4Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka

wakuposa mapiri muli achifwamba.

5Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao;

amuna onse amphamvu asowa manja ao.

6 Eks. 15.1, 21 Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,

galeta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo.

7 Nah. 1.6 Inu ndinu woopsa;

ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?

8 Ezk. 38.19-20 Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba;

dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete,

9pakuuka Mulungu kuti aweruze,

kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.

10 Eks. 9.16 Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani;

chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.

11 Mas. 50.14 Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;

onse akumzinga abwere nacho chopereka

cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.

12Iye adzadula mzimu wa akulu;

akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help