1Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2Deut. 2.5; Amo. 1.11Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kuphiri la Seiri, nulinenere molitsutsa;
3nuti nalo, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndiipidwa nawe phiri la Seiri, ndipo ndidzakutambasulira dzanja langa, ndi kukusanduliza lachipululu ndi lodabwitsa.
4Ndidzapasula midzi yako, nudzakhala lachipululu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5Mas. 137.7; Oba. 1.9-10Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israele kumphamvu ya lupanga m'nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza;
6Mas. 109.17chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndikukonzeratu uphedwe, ndi mwazi udzakulondola; popeza sunadana nao mwazi, mwazi udzakulondola.
7Ndipo ndidzaika phiri la Seiri lodabwitsa ndi lachipululu, ndi kuononga pomwepo wopitapo ndi wobwerapo.
8Ndipo ndidzadzaza mapiri ake ndi ophedwa ake pa zitunda zako, ndi m'zigwa zako, ndi m'mitsinje mwako monse; adzagwa ophedwa ndi lupanga.
9Ezk. 35.4Ndidzakusandutsa mabwinja osatha; ndi m'midzi mwako simudzakhalanso anthu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
10Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko;
11Mat. 7.2; Yak. 2.12-13chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndidzachita monga mwa mkwiyo wako, ndi monga mwa nsanje yako unachita nayo pa kukwiya nao iwe; ndipo ndidzadziwika nao pamene ndikuweruza.
12Ndipo udzadziwa kuti Ine Yehova ndidamva zamwano zako zonse udazinena pa mapiri a Israele, ndi kuti, Apasuka, apatsidwa kwa ife tiwadye.
131Sam. 2.3Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundichulukitsira mau anu ndawamva Ine.
14Yes. 65.13-14Atero Ambuye Yehova, Pokondwerera dziko lonse ndidzakusanduliza lachipululu.
15Oba. 12, 15Monga momwe unakondwerera cholowa cha nyumba ya Israele, popeza chidapasuka, momwemo ndidzakuchitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.