YOBU 7 - Buku Lopatulika Bible 2014

1Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno?

Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?

2Monga kapolo woliralira mthunzi,

monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,

3momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pake.

Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.

4 Deut. 28.67 Ndigona pansi, ndikuti,

Ndidzauka liti? Koma usiku undikulira;

ndipo ndimapalapata mpaka mbandakucha.

5Mnofu wanga wavala mphutsi ndi nkanambo zadothi;

khungu langa lang'ambika, nilinyansa.

6 Mas. 90.6-10 Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba,

apitirira opanda chiyembekezo.

7Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo,

diso langa silidzaonanso chokoma.

8Diso la amene andiona silidzandionanso,

maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.

9 2Sam. 12.23 Mtambo wapita watha,

momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.

10Sadzabweranso kunyumba yake,

osamdziwanso malo ake.

11 1Sam. 1.10 Potero sindidzaletsa pakamwa panga;

ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga;

ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.

12Ndine nyanja kodi, kapena chinjoka cha m'nyanja,

kuti Inu mundiikira odikira?

13Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,

pogona panga padzachepsa chondidandaulitsa;

14pamenepo mundiopsa ndi maloto,

nimundichititsa mantha ndi masomphenya;

15potero moyo wanga usankha kupotedwa,

ndi imfa, koposa mafupa anga awa.

16 Mas. 39.11 Ndinyansidwa nao moyo wanga;

sindidzakhala ndi moyo chikhalire;

mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.

17 Aheb. 2.6 Munthu ndani kuti mumkuze,

ndi kuti muike mtima wanu pa iye,

18ndi kuti mucheze naye m'mawa ndi m'mawa,

ndi kumuyesa nthawi zonse?

19Mukana kundichokera kufikira liti,

kapena kundileka mpaka nditameza dovu?

20Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani,

Inu wodikira anthu?

Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu?

Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?

21Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga

ndi kundichotsera mphulupulu yanga?

Popeza tsopano ndidzagona kufumbi;

mudzandifunafuna, koma ine palibe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help