1Ndipo mfumu Ahasuwero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja.
2Est. 9.4Ndi zochita zonse za mphamvu yake, ndi nyonga zake, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Mordekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Mediya ndi Persiya?
3Gen. 41.40; Neh. 2.10; Mas. 122.8-9Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.