CHIVUMBULUTSO 14 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mwanawankhosa ndi oomboledwa ake pa phiri la Ziyoni

1

13 1Ate. 4.16; 2Ate. 1.7 Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.

Masika a dzinthu ndi a mphesa

14 Ezk. 1.26; Chiv. 6.2 Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina monga Mwana wa Munthu, wakukhala naye korona wagolide pamutu pake, ndi m'dzanja lake chisenga lakuthwa.

15Mat. 13.39Ndipo mngelo wina anatuluka m'Kachisi, wofuula ndi mau akulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.

16Ndipo Iye wokhala pamtambo anaponya chisenga chake padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.

17Ndipo mngelo wina anatuluka m'Kachisi ali m'Mwamba, nakhala nacho chisenga chakuthwa nayenso.

18Yow. 3.13; Chiv. 16.8Ndipo mngelo wina anatuluka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; nafuula ndi mau akulu kwa iye wakukhala nacho chisenga chakuthwa, nanena, Tumiza chisenga chako chakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu.

19Chiv. 19.15Ndipo mngelo anaponya chisenga chake kudziko nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.

20Yes. 63.3; Aheb. 13.12Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mudzi, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help