EKSODO 11 - Buku Lopatulika Bible 2014

Chozizwitsa chakhumi: Imfa ya ana oyamba kubadwa

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.

2Eks. 3.22Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolide.

3Eks. 12.36Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m'dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.

4Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzatuluka Ine kunka pakati pa Aejipito;

5ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.

6Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m'dziko lonse la Ejipito, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere.

7Eks. 8.22Koma palibe galu adzafunyitsira lilime lake ana onse a Israele ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aejipito ndi Aisraele.

8Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.

9Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zichuluke m'dziko la Ejipito.

10Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m'dziko lake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help