1 MBIRI 21 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide awerenga anthu, mliri ugwera Israele

1 2Sam. 24.1-25 Pamenepo Satana anaukira Israele, nasonkhezera Davide awerenge Israele.

2Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa akulu a anthu, Kawerengeni Israele kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe chiwerengo chao.

3Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?

4Koma mau a mfumu anamlaka Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza ku Yerusalemu.

5Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga.

61Mbi. 27.24Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.

7Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi, chifukwa chake Iye anakantha Israele.

8Pamenepo Davide anati kwa Mulungu, Ndachimwa kwakukulu ndi kuchita chinthu ichi; koma tsopano, muchotse mphulupulu ya kapolo wanu, pakuti ndachita kopusa ndithu.

9Ndipo Yehova ananena ndi Gadi mlauli wa Davide, ndi kuti,

10Kanene kwa Davide kuti, Atero Yehova, Ndikuikira zitatu; dzisankhireko chimodzi ndikuchitire ichi.

11Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko;

12kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine?

13Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zake zichulukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.

14Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israele; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israele.

Davide amangira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani

15 Gen. 6.6 Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi.

16Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.

17Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri.

18Pamenepo mthenga wa Yehova anauza Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi.

19Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi adawanena m'dzina la Yehova.

20Pocheuka Orinani anaona wamthengayo; ndi ana ake amuna anai anali naye anabisala. Koma Orinani analikupuntha tirigu.

21Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, natuluka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yake pansi.

22Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse ili pa mtengo wake wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.

23Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu ichite chomkomera m'maso mwake; taonani, ndikupatsani ng'ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse.

24Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, Iai, koma ndidzaligula pa mtengo wake wonse; pakuti sindidzatengera Yehova chili chako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wake.

25Momwemo Davide anapatsa Orinani chogulira malowa golide wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwake.

26Lev. 9.24Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'Mwamba ndi moto pa guwa la nsembe yopsereza.

27Ndipo Yehova anauza wamthenga kuti abweze lupanga lake m'chimake.

28Nthawi yomweyi, pakuona Davide kuti Yehova anamvomereza pa dwale la Orinani Myebusi, anaphera nsembe pomwepo.

291Maf. 3.4Pakuti Kachisi wa Yehova amene Mose anapanga m'chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibiyoni nthawi yomweyi.

30Koma Davide sanathe kumuka kukhomo kwake kufunsira kwa Mulungu, pakuti anaopa lupanga la mthenga wa Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help