1Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga.
2Tamvetsani mau a kufuula kwanga,
Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga;
pakuti kwa Inu ndimapemphera.
3 Mas. 88.13 M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga;
m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
4Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa
mphulupulu siikhala ndi Inu.
5 Hab. 1.13 Opusa sadzakhazikika pamaso panu,
mudana nao onse akuchita zopanda pake.
6 Mas. 55.23 Mudzaononga iwo akunena bodza;
munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo,
Yehova anyansidwa naye.
7 1Maf. 8.29-30 Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu
ndidzalowa m'nyumba yanu;
ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
8 Mas. 25.5 Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu,
chifukwa cha akundizondawo;
mulungamitse njira yanu pamaso panga.
9 Mas. 62.4; Aro. 3.13 Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika;
m'kati mwao m'mosakaza;
m'mero mwao ndi manda apululu;
lilime lao asyasyalika nalo.
10 2Sam. 15.31 Muwayese otsutsika Mulungu;
agwe nao uphungu wao.
M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse;
pakuti anapikisana ndi Inu.
11 Yes. 65.13 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,
afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;
nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.
12Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;
mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.