1
12 1Ako. 3.13 Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu:
13Aro. 8.17-18; Afi. 3.10koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.
142Ako. 12.10Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.
151Pet. 2.20Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;
16Mac. 5.41koma akamva zowawa ngati mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili.
17Yer. 25.29; Mala. 3.5Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?
18Luk. 23.31Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?
192Tim. 1.12Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.