1Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka,
iwo amene atate ao ndikadawapeputsa,
osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga.
2Mphamvunso ya m'manja mwao ndikadapindulanji nayo?
Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha,
3atsala mafupa okhaokha ndi kusowa ndi njala;
akungudza nthaka youma kuli mdima wa m'chipululu chopasuka.
4Atchera therere lokolera kuzitsamba,
ndi chakudya chao ndicho mizu ya dinde.
5Anawapirikitsa pakati pa anthu,
awafuulira ngati kutsata mbala.
6Azikhala m'zigwa za chizirezire,
m'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga.
7Pakati pa zitsamba alira ngati bulu,
pansi pa khwisa asonkhana pamodzi.
8Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina;
anawaingitsa kuwachotsa m'dziko.
9 Mas. 69.12 Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo,
nandiyesa nthanthi.
10 Yes. 50.6; Mat. 26.67 Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine,
saleka kuthira malovu pankhope panga.
11Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza;
anataya chomangira m'kamwa mwao pamaso panga.
12Kudzanja langa lamanja anauka oluluka,
akankha mapazi anga,
andiundira njira zao zakundiononga.
13Aipsa njira yanga,
athandizana ndi tsoka langa;
ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi.
14Akudza ngati opitira pogamuka linga papakulu,
pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine.
15Anditembenuzira zondiopsa,
auluza ulemu wanga ngati mphepo;
ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo.
16 1Sam. 1.15; Mas. 42.3-4 Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m'kati mwanga;
masiku akuzunza andigwira.
17Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine,
ndi zowawa zondikungudza sizipuma.
18Mwa mphamvu yaikulu ya nthenda yanga
chovala changa chinasandulika,
chindithina ngati pakhosi pa malaya anga.
19Iye anandiponya m'matope,
ndipo ndafanana ndi fumbi ndi phulusa.
20Ndifuula kwa Inu, koma simundiyankha;
ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera.
21Mwasandulika kundichitira nkharwe;
ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.
22Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo;
ndipo mundisungunula mumkuntho.
23 Aheb. 9.27 Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa,
ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse.
24Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lake kodi?
Akati aonongeke, safuulako kodi?
25 Aro. 12.15 Kodi sindinamlirira misozi wakulawa zowawa?
Kodi moyo wanga sunachitira chisoni osowa?
26 Yer. 8.15 Muja ndinayembekeza chokoma chinadza choipa,
ndipo polindira kuunika unadza mdima.
27M'kati mwanga mupweteka mosapuma,
masiku a mazunzo andidzera.
28Ndiyenda ndili wothimbirira osati ndi dzuwa ai;
ndinyamuka mumsonkhano ndi kufuula.
29Ndili mbale wao wa ankhandwe,
ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.
30 Mali. 5.10 Khungu langa lada, nilindifundukira;
ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.
31Chifukwa chake zeze wanga wasandulika wa maliro,
ndi chitoliro changa cha mau a olira misozi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.