YOBU 41 - Buku Lopatulika Bible 2014

1Kodi ukhoza kukoka Leviyatani ndi mbedza?

Kapena kukanikiza kalandira wake ndi chingwe?

2Kodi ukhoza kumanga m'mphuno ndi mlulu?

Kapena kuboola nsagwada wake ndi mbedza?

3Kodi idzachulukitsa mau akukupembedza?

Kapena idzanena nawe mau ofatsa?

4Kodi idzapangana ndi iwe,

kuti uitenge ikhale kapolo wako wachikhalire?

5Kodi udzasewera nayo ngati mbalame?

Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete?

6Kodi opangana malonda adzaitsatsa?

Adzaigawana eni malonda?

7Kodi udzadzaza khungu lake ndi ntchetho,

kapena mutu wake ndi miomba?

8Isanjike dzanja lako;

ukakumbukira nkhondoyi, sudzateronso.

9Taona, chiyembekezo chako cha pa iyo chipita pachabe.

Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?

10Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa.

Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?

11 Mas. 50.12; Aro. 11.35 Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze?

Zilizonse pansi pa thambo ponse ndi zanga.

12Sindikhala chete osatchula ziwalo za ng'onayo,

ndi mbiri ya mphamvu yake, ndi makonzedwe ake okoma.

13Ndani adzasenda chovala chake chakunja?

Adzalowa ndani kumizere iwiri ya mano ake?

14Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pake?

Mano ake aopsa pozungulira pao.

15Mamba ake olimba ndiwo kudzitama kwake;

amangika pamodzi ngati okomeredwatu.

16Alumikizana lina ndi linzake,

mphepo yosalowa pakati pao.

17Amamatirana lina ndi linzake,

agwirana osagawanikana.

18Pakuyetsemula ing'anipitsa kuunika,

ndi maso ake akunga zikope za m'mawa.

19M'kamwa mwake mutuluka miuni,

mbaliwali za moto zibukamo.

20M'mphuno mwake mutuluka utsi,

ngati nkhali yobwadamuka ndi moto wa zinyatsi

21mpweya wake uyatsa makala,

ndi m'kamwa mwake mutuluka lawi la moto.

22Kukhosi kwake kukhala mphamvu,

ndi mantha avumbuluka patsogolo pake.

23Nyama yake yopsapsala igwirana

ikwima pathupi pake yosagwedezeka.

24Mtima wake ulimba ngati mwala,

inde ulimba ngati mwala wa mphero.

25Ikanyamuka, amphamvu achita mantha;

chifukwa cha kuopsedwa azimidwa nzeru.

26Munthu akaiyamba ndi lupanga, ligoma;

ngakhale nthungo, kapena muvi, kapena mkondo.

27Chitsulo ichiyesa phesi,

ndi mkuwa ngati mtengo woola.

28Muvi suithawitsa,

miyala ya pachoponyera iisandutsa chiputu.

29Zibonga ziyesedwa chiputu,

iseka kuthikuza kwake kwa nthungo.

30Kumimba kwake ikunga mapale akuthwa,

itasalala kuthope ngati chopunthira.

31Ichititsa nthubwinthubwi pozama ngati nkhali,

isanduliza nyanja ikunge mafuta.

32Ichititsa mifunde yonyezimira pambuyo pake;

munthu akadati pozama pali ndi imvi.

33Pa dziko lapansi palibe china cholingana nayo,

cholengedwa chopanda mantha.

34Ipenya chilichonse chodzikuza,

ndiyo mfumu ya zodzitama zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help