ESTERE 2 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ahasuwero akwatira Estere

1Zitatha izi, utaleka mkwiyo wa mfumu Ahasuwero, anakumbukira Vasiti, ndi chochita iye, ndi chomlamulidwira.

2Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola;

3ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'chinyumba cha ku Susa, m'nyumba ya akazi; awasunge Hegai mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;

4ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti. Ndipo chinthuchi chinamkonda mfumu, nachita chomwecho.

5Panali Myuda m'chinyumba cha ku Susa, dzina lake ndiye Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi Mbenjamini;

62Maf. 24.14-15uyu anatengedwa ndende ku Yerusalemu, pamodzi ndi andende anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adamtenga ndende.

7Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wake wamng'ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wake ndi mai wake, Mordekai anamtenga akhale mwana wake.

8Ndipo kunali, atamveka mau a mfumu ndi lamulo lake, ndipo atasonkhanidwa anamwali ambiri m'chinyumba cha ku Susa, awasunge Hegai, anamtenga Estere yemwe, alowe m'nyumba ya mfumu, amsunge Hegai wosunga akazi.

9Ndipo namwaliyo anamkomera, namchitira chifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zake zomyeretsa, ndi magawo ake, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ochokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ake akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi.

10Estere sadawulula mtundu wake ndi chibale chake; pakuti Mordekai adamuuzitsa kuti asadziwulule.

11Ndi Mordekai akayendayenda tsiku ndi tsiku kubwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi chimene chidzamchitikira.

12Kunafika tsono kulowa kwake kwa namwali aliyense, kuti alowe kwa mfumu Ahasuwero, atamchitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti ankakwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.

13Ndipo namwali aliyense analowa kwa mfumu motero, zilizonse anafuna anampatsa zochokera m'nyumba ya akazi, alowe nazo kunyumba ya mfumu.

14Madzulo ake analowamo, nabwera m'mawa mwake kunka kunyumba yachiwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi aang'ono a mfumu; iyeyu sanalowenso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumtchula dzina lake, ndiko.

15Pofika tsono kulowa kwake kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Mordekai, amene adadzitengera akhale mwana wake, kuti alowe kwa mfumu, sanafune kanthu koma zonena Hegai mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.

16Momwemo anatengedwa Estere kunka kwa mfumu Ahasuwero, kunyumba yake yachifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebeti, chaka chachisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.

17Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi chifundo pamaso pake, koposa anamwali onse; motero anaika korona wachifumu pamutu pake, namuyesa mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti.

18Est. 1.3Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akulu ake onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.

19Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yachiwiri Mordekai anali wa m'bwalo la mfumu.

20Estere sadawulula chibale chake kapena mtundu wake, monga Mordekai adamuuza; popeza Estere anachita mau a Mordekai monga m'mene analeredwa naye.

Mordekai awulula chiwembu chofuna kupha mfumu

21Masiku awa pokhala Mordekai wa m'bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.

22Est. 6.2Koma chidadziwika ichi kwa Mordekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkulu; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Mordekai.

23Est. 6.1Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napachikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anachilemba m'buku la mbiri pamaso pa mfumu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help