1 TIMOTEO Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014

Mau OyambaTimoteo anali mkhristu wachinyamata wa ku Asiya, mai wake anali Myuda koma bambo wake anali Mgriki. Paulo adamtenga kuti amperekeze pa maulendo ake ndi kumthandiza pa ntchito yolalika. Pomulembera kalatayi, Paulo afuna kumchenjeza pa zophunzitsa zina zabodza zimene zikusokoneza mpingo. Anthu ena ophatikiza nzeru zina zachiyuda ndi zina zachikunja ankati dziko lapansi monga lilirimu nloipa, ndipo palibe munthu angapulumuke akapanda kuphunzira nzeru zina zobisika ndi kutsata miyambo ina, monga kusala zakudya zina ndi zina ndi kuletsa maukwati. Paulo akuperekanso malangizo pa chipembedzo, za kayendetsedwe ka mpingo ndi za makhalidwe ofunika kwa atsogoleri. Akumuuzanso kuti iye ayesetse kukhala mtumiki wokhulupirika pa udindo wake woyang'anira magulu onse a Akhristu.Za mkatimuMau oyamba 1.1-2Malangizo okhudza mpingo ndi atsogoleri ake 1.3—3.16Malangizo kwa Timoteo pa ntchito yake 4.1—6.21
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help