YOBU 37 - Buku Lopatulika Bible 2014

1Pa ichinso mtima wanga unjenjemera,

nusunthika m'malo mwake.

2Mvetsetsani chibumo cha mau ake,

ndi kugunda kotuluka m'kamwa mwake.

3Akumveketsa pansi pa thambo ponse,

nang'anipitsa mphezi yake ku malekezero a dziko lapansi.

4 Mas. 29.3-4 Mau abuma kuitsata,

agunda ndi mau a ukulu wake,

ndipo sailetsa atamveka mau ake.

5Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ake,

achita zazikulu osazidziwa ife.

6 Mas. 147.16-18 Pakuti anena kwa chipale chofewa, Ugwe padziko,

momwemonso kwa mvula,

ndi kwa mvumbi waukulu.

7Atsekereza mokhomera chizindikiro dzanja la munthu aliyense,

kuti anthu onse anawalenga adziwe.

8Pamenepo zilombo zilowa mobisalamo,

nizikhala m'ngaka mwao.

9M'chipinda mwake mutuluka kamvulumvulu,

ndi chisanu chifuma kumpoto.

10 Mas. 147.16-18 Mwa kupuma kwake Mulungu apereka chipale,

ndi madzi achitando aundana.

11Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi,

afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yake;

12 Mas. 148.8, 13 ndipo utembenukatembenuka pakulangiza kwake,

kuti uchite zilizonse aulamulira,

pa nkhope ya dziko lokhalamo anthu;

13 1Sam. 12.18-19 ngati aufikitsira dziko lake kulidzudzula,

kapena kulichitira chifundo.

14 Mas. 111.2 Tamverani ichi, Yobu.

Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu.

15Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi,

nawalitsa mphezi ya m'mtambo mwake?

16Kodi mudziwa madendekeredwe ake a mitambo,

zodabwitsa za Iye wakudziwa mwangwiro?

17Kodi mudziwa umo zovala zanu zifundira,

pamene dziko lili thuu chifukwa cha mwera?

18 Yes. 44.24 Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye,

ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka?

19Mutilangize chimene tidzanena ndi Iye;

sitidziwa kulongosola mau athu chifukwa cha mdima.

20Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena,

kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa?

21Ndipo tsopano anthu sakhoza kupenyerera kuunika

pakunyezimira kuthambo,

ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa.

22Kuchokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira,

Mulungu ali nao ukulu woopsa.

23 1Tim. 6.16 Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule;

ndiye wa mphamvu yoposa;

koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.

24 Mat. 10.28 M'mwemo anthu amuopa,

Iye sasamalira aliyense wanzeru mumtima.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help