NUMERI 7 - Buku Lopatulika Bible 2014

Zopereka za Akulu 12 atautsa chihemacho

1 Eks. 40.18 Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa Kachisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;

2akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;

3anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa Kachisi.

4Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

5Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakuchitira ntchito ya chihema chokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa ntchito yake.

6Ndipo Mose analandira magaleta ndi ng'ombe, nazipereka kwa Alevi.

7Anapatsa ana a Geresoni magaleta awiri ndi ng'ombe zinai, monga mwa ntchito yao;

8napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.

9Koma sanapatse ana a Kohati kanthu; popeza ntchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.

10Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka chiperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera nacho chopereka chao pa guwa la nsembelo.

11Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lake, apereke zopereka zao za kupereka chiperekere guwa la nsembe.

12Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda:

13chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;

14chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

15ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

16tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

17ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Nasoni mwana wa Aminadabu.

18Tsiku lachiwiri Netanele mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera nacho chake:

19anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

20chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

21ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

22tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

23ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Netanele mwana wa Zuwara.

24Tsiku lachitatu kalonga wa ana a Zebuloni, ndiye Eliyabu mwana wa Heloni:

25chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

26chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

27ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

28tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

29ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyabu mwana wa Heloni.

30Tsiku lachinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni:

31chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

32chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

33ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

34tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

35ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri.

36Tsiku lachisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiele, mwana wa Zurishadai:

37chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

38chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

39ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

40tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

41ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Selumiele mwana wa Zurishadai.

42Tsiku lachisanu ndi chimodzi kalonga wa ana a Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele:

43chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu; mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

44chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

45ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

46tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

47ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuwele.

48Tsiku lachisanu ndi chiwiri kalonga wa ana a Efuremu Elisama mwana wa Amihudi:

49chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

50chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

51ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

52tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

53ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa za mphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Elisama mwana wa Amihudi.

54Tsiku lachisanu ndi chitatu kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliele mwana wa Pedazuri:

55chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

56chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

57ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

58tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

59ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Gamaliele mwana wa Pedazuri.

60Tsiku lachisanu ndi chinai kalonga wa ana a Benjamini, ndiye Abidani mwana wa Gideoni:

61chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

62chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

63ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

64tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

65ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni.

66Tsiku lakhumi kalonga wa ana a Dani, ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai:

67chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;

68chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

69ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

70tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

71ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Ahiyezere mwana wa Amisadai.

72Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Asere, ndiye Pagiyele mwana wa Okarani;

73chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

74chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

75ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

76tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

77ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Pagiyele mwana wa Okarani.

78Tsiku lakhumi ndi chiwiri kalonga wa ana a Nafutali, ndiye Ahira mwana wa Enani:

79chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

80chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

81ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

82tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;

83ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ichi ndi chopereka cha Ahira mwana wa Enani.

84Uku ndi kupereka chiperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israele, tsiku la kudzoza kwake: mbale zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolide khumi ndi ziwiri;

85mbale yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.

86Zipande zagolide ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi chofukiza, chipande chonse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golide wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;

87ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, anaankhosa a chaka chimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zauchimo khumi ndi awiri;

88ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.

89Eks. 25.22; 33.9Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help