NUMERI 25 - Buku Lopatulika Bible 2014

Aisraele achita chigololo napembedza mafano ku Sitimu

1 1Ako. 10.8 Ndipo Israele anakhala m'Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana akazi a Mowabu;

2Yos. 22.17; Hos. 9.10popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.

3Pamene Israele anaphatikana ndi Baala-Peori, Yehova anapsa mtima pa Israele.

4Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akulu onse a anthu nuwapachikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova uchoke kwa Israele.

5Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori.

6Yow. 2.17Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo la chihema chokomanako.

7Pamene Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anachiona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lake;

8natsata munthu Mwisraele m'hema, nawamoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m'mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele.

9Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.

10Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

11Zef. 1.18; 2Ako. 11.2Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israele m'nsanje yanga.

12Mala. 2.4-5Chifukwa chake nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;

13ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.

14Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni.

15Ndi dzina la mkazi Mmidiyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkulu wa anthu a nyumba ya makolo m'Midiyani.

16Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

17Sautsa Amidiyani ndi kuwakantha;

18popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'chija cha Peori.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help