2 TIMOTEO 1 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 2Ako. 1.1 Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Khristu Yesu,

21Tim. 1.2kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.

Chikondi cha Paulo cha pa Timoteo

3 Mac. 24.14; Aro. 1.9 Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbu mtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,

4pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndidzazidwe nacho chimwemwe;

5Mac. 16.1; 1Tim. 1.5pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.

61Tim. 4.14Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.

7Luk. 24.49Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

8Aro. 1.16; Akol. 1.24Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;

9Aro. 8.28; 1Ate. 4.7amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,

101Ako. 15.54-55; Aef. 1.9koma chaonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino,

111Tim. 2.7umene ndaikikapo mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wake.

122Tim. 2.9; 1Pet. 4.19Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.

132Tim. 3.14Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.

14Aro. 8.11; 1Tim. 6.20Chosungitsa chokomacho udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.

15 2Tim. 4.10, 16 Ichi uchidziwa, kuti onse a m'Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Figelo ndi Heremogene.

16Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachita manyazi ndi unyolo wanga;

17komatu pokhala m'Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza.

18Mat. 25.34-40(Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help