1 2Maf. 1.12; Mas. 78.21 Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.
2Pamenepo anthu anafuulira kwa Mose; ndi Mose anapemphera kwa Yehova, ndi motowo unazimika.
3Ndipo anatcha malowo dzina lake Tabera; popeza moto wa Yehova udayaka pakati pao.
4 1Ako. 10.6 Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?
5Tikumbukira nsomba tinazidya m'Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi a mitundu itatu;
6koma tsopano moyo wathu waphwa; tilibe kanthu pamaso pathu koma mana awa.
7Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ake ngati maonekedwe a bedola.
8Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.
9Ndipo pakugwa mame pachigono usiku, mana anagwapo.
Mose adandaula pa katundu wake10Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.
11Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munachitiranji choipa mtumiki wanu? Ndalekeranji kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse?
12Yes. 40.11; 1Ate. 2.7Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?
13Mat. 15.33Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? Pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye.
14Eks. 18.18Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine.
151Maf. 19.4; Yon. 4.3Ndipo ngati mundichitira chotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang'ane tsoka langa.
16 Eks. 24.1, 9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.
171Sam. 10.6; 2Maf. 2.9, 15Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.
18Num. 11.5; Mac. 7.39Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino m'Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya.
19Simudzadya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku khumi, kapena masiku makumi awiri;
20koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji m'Ejipito?
21Ndipo Mose anati, Anthu amene ndili pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.
222Maf. 7.2; Mrk. 8.4Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? Kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira?
23 Yes. 59.1; Ezk. 24.14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? Tsopano udzapenya ngati mau anga adzakuchitikira kapena iai.
24Ndipo Mose anatuluka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akulu a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa chihema.
25Yow. 2.28Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.
26Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono.
27Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'chigono.
28Mrk. 9.38Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.
291Ako. 14.5Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!
30Ndipo Mose ndi akulu onse a Israele anasonkhana kuchigono.
31Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zochokera kunyanja, nizitula kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.
32Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono.
33Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.
34Ndipo anatcha malowo dzina lake Kibroti-Hatava; popeza pamenepo anaika anthu osusuka.
35Kuchokera ku Kibroti-Hatava anthuwo anayenda kunka ku Hazeroti; nakhala ku Hazeroti.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.