1 Yon. 4.3, 8 Mtima wanga ulema nao moyo wanga,
ndidzadzilolera kudandaula kwanga,
ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.
2Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse;
mundidziwitse chifukwa cha kutsutsana nane.
3Chikukomerani kodi kungosautsa,
kuti mupeputsa ntchito yolemetsa manja anu,
ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?
4 1Sam. 16.7 Muli nao maso a thupi kodi?
Mupenya kodi monga umo apenyera munthu?
5Masiku anu akunga masiku a munthu kodi,
zaka zanu zikunga masiku a munthu;
6kuti mufunsa mphulupulu yanga,
ndi kulondola choipa changa;
7chinkana mudziwa kuti sindili woipa,
ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?
8 Mas. 119.73 Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu,
koma mufuna kundiononga.
9Mukumbukire kuti mwandiumba ngati dothi;
ndipo kodi mudzandibwezera kufumbi?
10Simunanditsanula kodi ngati mkaka,
ndi kundilimbitsa ngati mase?
11Munandiveka khungu ndi mnofu,
ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha.
12Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima,
ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga.
13Koma izi munazibisa mumtima mwanu;
ndidziwa kuti ichi muli nacho.
14 Mas. 139.1 Ndikachimwa mundipenya;
ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga.
15 Yes. 3.11 Ndikakhala woipa, tsoka ine;
ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutu wanga;
ndadzazidwa ndi manyazi,
koma penyani kuzunzika kwanga.
16Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango;
mubweranso ndi kudzionetsera modabwitsa kwa ine.
17Mundikonzeranso mboni zonditsutsa,
ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu;
nkhondo yobwerezabwereza yandigwera.
18 Yob. 3.11 Potero munandibadwitsa chifukwa ninji?
Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso.
19Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala;
akadanditenga pobadwapo kunka nane kumanda.
20 Mas. 39.13 Masiku anga satsala owerengeka nanga? Lindani.
Bandilekani kuti nditsitsimuke pang'ono,
21 Mas. 88.12 ndisanachoke kunka kumene sindikabweranso,
ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa.
22Dziko la mdima bii ngati mdima wandiweyani,
dziko la mthunzi wa imfa losalongosoka,
kumene kuunika kukunga mdima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.