MALAKI 1 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kusayamika kwa Israele pa chikondi cha Mulungu

1Katundu wa mau a Yehova wa kwa Israele mwa Malaki.

2Deut. 7.8; Aro. 9.13Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;

3koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m'chipululu.

4Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.

5Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.

6 Eks. 20.12; Luk. 6.46 Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?

7Deut. 15.21Mupereka mkate wodetsedwa pa guwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.

8Lev. 22.22Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.

9Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.

10Yer. 6.20Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu.

11Mas. 113.3; Yes. 59.19; 66.19Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

12Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.

13Lev. 22.22Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.

14Mas. 47.2; Mala. 1.8; 1Tim. 6.15Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help