MASALIMO 54 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide apempha Mulungu amlanditseKwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Chilangizo cha Davide. Muja Azifi anamuka nauza Saulo, kuti, Kodi Davide sabisala kwathu nanga?

1Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu,

ndipo mundiweruze ndi mphamvu yanu.

2Imvani pemphero langa, Mulungu;

tcherani khutu mau a pakamwa panga.

3 Mas. 86.14 Pakuti alendo andiukira,

ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;

sadziikira Mulungu pamaso pao.

4 Mas. 118.7 Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga,

Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.

5Adzabwezera choipa adani anga,

aduleni m'choonadi chanu.

6Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu,

ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.

7Pakuti anandilanditsa m'nsautso yonse;

ndipo ndapenya ndi diso langa icho ndakhumbira pa adani anga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help