LEVITIKO 27 - Buku Lopatulika Bible 2014

Chowinda ndi chiombolo chake

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2Num. 6.2; Ower. 11.30; 1Sam. 1.11Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene munthu achita chowinda cha padera, anthuwo azikhala a Yehova monga mwa kuyesa kwako.

3Ukayesa wamwamuna wa zaka makumi awiri kufikira wina wa zaka makumi asanu ndi limodzi, uziwayesera a masekeli makumi asanu a siliva, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

4Koma akakhala wamkazi, umuyesere wa masekeli makumi atatu.

5Akakhala munthu wa zaka zisanu kufikira wina wa zaka makumi awiri uwayesere, wamwamuna wa masekeli makumi awiri, ndi wamkazi wa masekeli khumi.

6Akakhala mwana wa mwezi umodzi kufikira zaka zisanu, uziwayesera wamwamuna wa masekeli asanu a siliva, ndi wamkazi wa masekeli atatu a siliva.

7Akakhala munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu, akakhala wamwamuna, umuyesere wa masekeli khumi ndi asanu, akakhala wamkazi wa masekeli khumi.

8Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.

9Ndipo chikakhala cha nyama imene anthu amabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.

10Asaisinthe, yokoma m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yokoma; ndipo akasinthadi nyama m'malo mwa inzake, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika.

11Ndipo chikakhala cha nyama yodetsa, imene sabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, aike nyamayi pamaso pa wansembe;

12ndipo wansembeyo aiyese mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga uiyesa wansembewe, momwemo.

13Ndipo akaiombola ndithu, pamenepo aonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake.

14Munthu akapatula nyumba yake ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.

15Ndipo iye wakuipatula akaombola nyumba yake, aonjezepo limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo idzakhala yake.

16Munthu akapatulirako Yehova munda wakewake, uziuyesa monga mwa mbeu zake zikakhala; homeri wa barele uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.

17Akapatula munda wake kuyambira chaka choliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.

18Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako.

19Ndipo wakupatula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wake.

20Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;

21koma potuluka m'chaka choliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; ukhale wakewake wa wansembe.

22Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wakewake;

23pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wake wa kuyesa kwako kufikira chaka choliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, chikhale chinthu chopatulikira Yehova.

24Lev. 25.28Chaka choliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lakelake.

25Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika sekeli ndi magera makumi awiri.

26 Eks. 13.2 Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.

27Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako.

Za choperekedwa chiperekere, ndi lakhumi la za nthaka ndi za m'khola

28Koma asachigulitse kapena kuchiombola chinthu choperekedwa chiperekere kwa Mulungu, chimene munthu achipereka chiperekere kwa Yehova, chotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wakewake; chilichonse choperekedwa chiperekere kwa Mulungu nchopatulika kwambiri.

29Ower. 11.35Asamuombole munthu woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu.

30 Gen. 28.22; 2Mbi. 31.5, 6; Mala. 3.8 Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.

31Koma munthu akaombolatu kanthu ka limodzi la magawo khumiwo aonjezeko limodzi la magawo asanu.

32Yer. 33.13; Ezk. 20.37Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, zilizonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhala lopatulikira Yehova.

33Asafunse ngati yabwino kapena yoipa, kapena kuisintha; koma akaisinthatu, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika zonse ziwiri; asamaiombola.

34Awa ndi malamulo, amene Yehova anauza Mose, awauze ana a Israele, m'phiri la Sinai.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help