YESAYA 48 - Buku Lopatulika Bible 2014

Awadandaulira Aisraele, awachenjeza, nalonjezana nao

1 Yer. 5.2 Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m'zoona, pena m'chilungamo.

2Aro. 2.17-23Pakuti adziyesa okha a mudzi wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu.

3Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazichita izo, ndipo zinaoneka.

4Eks. 32.9Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;

5chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira.

6Iwe wachimva; taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzachinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kuchokera nthawi yino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.

7Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa.

8Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.

9Mas. 78.38Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse.

10Mas. 66.10; 1Pet. 1.7Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.

11Yes. 42.8; 43.25; Ezk. 20.9Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.

12 Yes. 41.4 Mverani Ine, Yakobo ndi Israele, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womaliza.

13Mas. 102.25Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.

14Yes. 44.28Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni.

15Yes. 45.1-3Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yake.

16Yes. 61.1Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.

17Mas. 32.8Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.

18Mas. 81.13; 119.165Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;

19Gen. 22.17; Hos. 1.10mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m'chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.

20 Yes. 44.22-23; 52.11 Tulukani inu m'Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo.

21Deut. 8.15Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.

22Yes. 57.21Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help