1Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
2Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni.
3Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!
4Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?
5Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa m'Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.
6Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kunka ku khomo la chihema chokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.
7Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
8Eks. 17.5Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.
9Ndipo Mose anatenga ndodoyo kuichotsa pamaso pa Yehova, monga Iye anamuuza iye.
10Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nao iye, Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m'thanthwe umu?
111Ako. 10.4Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe.
12Ezk. 20.41; 1Pet. 3.15Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israele, chifukwa chake simudzalowetsa msonkhano uwu m'dziko ndinawapatsali.
13Mas. 95.8Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.
Mose apempha njira kwa Aedomu14 Gen. 36.31, 43; Oba. 1.10, 12 Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;
15Gen. 46.6kuti makolo athu anatsikira kunka ku Ejipito, ndipo tinakhala m'Ejipito masiku ambiri; ndipo Aejipito anachitira zoipa ife, ndi makolo athu.
16Eks. 14.19Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa m'Ejipito; ndipo, taonani, tili m'Kadesi, ndiwo mudzi wa malekezero a malire anu.
17Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.
18Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga.
19Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.
20Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anatulukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.
21Potero Edomu anakana kulola Israele kupitira pa malire ake; chifukwa chake Aisraele anampatukira.
Imfa ya Aroni22Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori.
23Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti,
24Num. 20.12Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.
25Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m'phiri la Hori;
26nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko.
27Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse.
28Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba pa phiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.
29Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.