1 Aro. 8.16; 1Yoh. 3.1; Agal. 3.26 Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pa maso chifukwa cha akufa.
2Deut. 7.6Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi.
3 Mac. 10.13-14 Musamadya chonyansa chilichonse.
4Nyamazi muyenera kumadya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, ndi mbuzi,
5ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.
6Ndipo nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya.
7Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda: ngamira, ndi kalulu, ndi mbira, popeza zibzikula, koma zosagawanika chiboda, muziyese zodetsa;
8ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.
9Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba, zimenezi muyenera kumadya;
10koma zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa.
11Mbalame zosadetsa zonse muyenera kumadya.
12Koma izi ndi zimene simuyenera kumadya: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi,
13ndi kamtema, ndi mphamba, ndi muimba monga mwa mtundu wake;
14ndi khungubwi aliyense monga mwa mtundu wake;
15ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi monga mwa mtundu wake;
16ndi nkhutukutu, ndi manchichi, ndi tsekwe;
17ndi vuwo, ndi dembo, ndi nswankhono;
18ndi indwa, ndi chimeza, monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme.
19Ndipo zokwawa zonse zakuuluka muziyesa zonyansa; musamazidya.
20Mbalame zonse zosadetsa muyenera kumadya.
21 Deut. 7.6 Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Za limodzi mwa magawo khumi22 Lev. 27.30 Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka.
23Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo Iye, kukhalitsamo dzina lake; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.
24Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lake, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;
25pamenepo mulisinthe ndalama, ndi kumanga ndalama ikhale m'dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;
26ndipo mugule ndi ndalamazo chilichonse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena chakumwa cholimba, kapena chilichonse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.
27Num. 18.20, 24; Deut. 12.19Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.
28Pakutha pake pa zaka zitatu muzitulutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za chaka icho, ndi kuwalinditsa m'mudzi mwanu;
29Deut. 15.10; Miy. 3.9, 10; Mala. 3.10ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.