YESAYA 17 - Buku Lopatulika Bible 2014

Aneneratu za Damasiko ndi Efuremu

1 Yer. 49.23-27; Amo. 1.3-5; 2Maf. 16.9 Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mudzi, ndimo udzangokhala muunda wopasudwa.

2Yer. 7.33Midzi ya Aroere yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsa.

3Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu.

4Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lake kudzaonda.

5Yer. 51.33Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu.

6Yes. 24.13Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo wa azitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.

7Mik. 7.7Tsiku limenelo munthu adzayang'ana kwa Mlengi wake, ndipo maso ake adzalemekeza Woyera wa Israele.

8Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.

9Tsiku limenelo midzi yake yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga pa phiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israele; ndipo padzakhala bwinja.

10Mas. 106.21Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo;

11tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.

Aneneratu za kufafanizika kwa nkhondo ya Asiriya

12 Yer. 6.23 Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu!

13Mas. 9.5; Hos. 13.3Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.

14Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanake, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help