1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2Lev. 18.21Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala m'Israele, amene apereka mbeu zake kwa Moleki, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.
3Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.
4Ndipo ngati anthu a m'dzikomo akambisa munthuyo pang'ono ponse, pamene apereka a mbeu zake kwa Moleki, kuti asamuphe;
5pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.
6Lev. 19.31Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.
7Lev. 19.2Chifukwa chake dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
8Ndipo musunge malemba anga ndi kuwachita; Ine ndine Yehova wakupatula inu.
9Miy. 20.20; Mat. 15.4Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.
10Yoh. 8.5Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.
11Munthu akagona naye mkazi wa atate wake, wavula atate wake; awaphe ndithu onse awiri; mwazi wao ukhale pamutu pao.
12Munthu akagona ndi mpongozi wake, awaphe onse awiri; achita chisokonezo; mwazi wao ukhale pamtu pao.
13Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.
14Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wake chochititsa manyazi ichi; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale chochititsa manyazicho pakati pa inu.
15Mwamuna akagona ndi nyama amuphe ndithu; muiphenso nyamayi.
16Mkazi akasendera kwa nyama iliyonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.
17Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake.
18Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakamvula, anavula kasupe wake, ndi iye mwini anavula kasupe wa nthenda yake; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.
19Usamavula mbale wa mai wako, kapena mlongo wa atate wako; popeza anavula abale ake; asenze mphulupulu yao.
20Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa atate wake, navula mbale wa atate wake; asenze kuchimwa kwao; adzafa osaona ana.
21Munthu akatenga mkazi wa mbale wake, chodetsa ichi; wavula mbale wake; adzakhala osaona ana.
22 Lev. 18.26 Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo.
23Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao.
24Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu.
25Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.
26Lev. 19.2Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.
27Lev. 19.31Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamtu pao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.