2 AKORINTO 7 - Buku Lopatulika Bible 2014

Paulo akondwera pa kudza kwa Tito, ndi pa zipatso za kalata wake woyamba

1 2Ako. 6.17-18; 1Yoh. 3.3 Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.

2 Mac. 20.33-34 Tipatseni malo; sitinamchitira munthu chosalungama, sitinaipsa munthu, sitinachenjerera munthu.

32Ako. 6.11-12Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.

42Ako. 1.4; Akol. 1.24Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.

5 2Ako. 2.13; 4.8 Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.

62Ako. 1.4Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;

7koma si ndi kufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene anatonthozedwa nacho mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, changu chanu cha kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa.

8Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.

9Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kalikonse.

102Sam. 12.13; Mat. 26.75Pakuti chisoni cha kwa Mulungu titembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.

11Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.

12Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.

13Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m'chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.

14Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.

152Ako. 2.9Ndipo chikondi chenicheni chake chichulukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.

162Ate. 3.4Ndikondwera kuti m'zonse ndilimbika mtima za inu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help