MALIRO 5 - Buku Lopatulika Bible 2014

Adandaulira Yehova pa tsoka la ukapolo wao

1Yehova, kumbukirani chotigwerachi,

penyani nimuone chitonzo chathu.

2Cholowa chathu chasanduka cha alendo,

ndi nyumba zathu za achilendo.

3Ndife amasiye opanda atate,

amai athu akunga akazi amasiye.

4Tinamwa madzi athu ndi ndalama,

tiona nkhuni zathu pozigula.

5

ndi anamwali m'midzi ya Yuda.

12Anawapachika akalonga manja ao;

sanalemekeze nkhope za akulu.

13Anyamata ananyamula mphero,

ana nakhumudwa posenza nkhuni.

14Akulu adatha kuzipata,

anyamata naleka nyimbo zao.

15Chimwemwe cha mtima wathu chalekeka,

masewera athu asanduka maliro.

16Korona wagwa pamutu pathu;

kalanga ife! Pakuti tinachimwa.

17Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka,

chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi;

18pa phiri la Ziyoni lopasukalo

ankhandwe ayendapo.

19 Mas. 9.7; 45.6; Hab. 1.12 Inu, Yehova, mukhala chikhalire,

ndi mpando wanu wachifumu ku mibadwomibadwo.

20 Mas. 13.1 Bwanji mutiiwala chiiwalire,

ndi kutisiya masiku ambirimbiri.

21 Mas. 80.3, 7, 19 Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova,

ndipo tidzatembenuzidwadi,

mukonzenso masiku athu ngati kale lija.

22Koma mwatikaniza konse,

mwatikwiyira kopambana.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help