2 MBIRI 12 - Buku Lopatulika Bible 2014

Sisake wa ku Ejipito athira nkhondo Rehobowamu

1 1Maf. 14.22-25; 2Mbi. 11.17 Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye.

2Ndipo Rehobowamu atakhala mfumu zaka zinai, Sisake mfumu ya ku Ejipito anakwerera Yerusalemu, popeza iwo adalakwira Yehova.

3Anakwera ndi magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kutuluka m'Ejipito ngosawerengeka, Alibiya, Asuki, ndi Akusi.

4Ndipo analanda midzi yamalinga yokhala ya Yuda, nadza ku Yerusalemu.

51Maf. 12.22Pamenepo Semaya mneneri anadza kwa Rehobowamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, chifukwa chake Inenso ndasiya inu m'dzanja la Sisake.

6Pamenepo akalonga a Israele ndi mfumu anadzichepetsa, nati, Yehova ali wolungama.

7Yak. 4.10; 1Maf. 21.28-29Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake.

8Yes. 26.13Koma adzakhala akapolo ake, kuti adziwe kunditumikira kwanga, ndi kuwatumikira kwa maufumu a maiko.

Sisake alanda chuma cha Kachisi ndi cha nyumba ya mfumu

9 1Maf. 10.16-17; 14.25-26 Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni.

10Ndipo Rehobowamu mfumu anapanga m'malo mwa izi zikopa zamkuwa, nazipereka m'manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

11Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku chipinda cha olindirira.

12Ndipo pakudzichepetsa iye mkwiyo wa Yehova unamchokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma m'Yuda.

13Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu m'Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, ndiwo mudzi Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.

14Koma anachita choipa, popeza sanalunjikitse mtima wake kufuna Yehova.

151Maf. 14.30-31Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse.

16Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide; ndipo Abiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help