YESAYA 41 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yehova yekha ndiye Mulungu, Israele amkhulupirire Iye yekhayekha

1 Zek. 2.13 Khalani chete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni tiyandikire pamodzi kuchiweruziro.

2Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.

3Iye awathamangitsa, napitirira mwamtendere; pa njira imene asanapitemo ndi mapazi ake.

4Yes. 43.10; Chiv. 22.13Ndani wachipanga, nachimaliza icho, kutchula mibadwo chiyambire? Ine Yehova, ndine ndemwe.

5Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.

6Iwo anathangata yense mnansi wake, ndi yense anati kwa mbale wake, Khala wolimba mtima.

7Yes. 40.19Chotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golide, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi ntovu, Kuli kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.

8 Deut. 7.6; 2Mbi. 20.7; Yak. 2.23 Koma iwe, Israele, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;

9iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kuchokera m'ngodya zake, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja;

10Deut. 31.6, 8usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

11Eks. 23.22Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati chabe, nadzaonongeka.

12Iwe udzawafuna osawapeza, ngakhale iwo amene akangana ndi iwe; ochita nkhondo ndi iwe, adzakhala ngati chabe, ndi monga kanthu kopanda pake.

13Yes. 41.10Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.

14Mas. 78.35; Yes. 54.5Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.

15Mik. 4.13Taona, ndidzakuyesa iwe choombera tirigu chatsopano chakuthwa chokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.

16Yer. 51.2Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.

17Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.

18Mas. 107.35; Yes. 35.6-7Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti see, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa chipululu, chikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.

19Ndidzabzala m'chipululu mkungudza, ndi msangu, ndi kasiya, ndi mtengo wa azitona; ndidzaika m'chipululu pamodzi mlombwa, ndi mkuyu, ndi naphini;

20Yob. 12.9kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lachita ichi, ndipo Woyera wa Israele wachilenga ichi.

21Onetsani mlandu wanu, ati Yehova; tulutsani zifukwa zanu zolimba, ati mfumu ya Yakobo.

22Azitulutse, atitchulire ife, chimene chidzaoneka; tchulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziwa mamaliziro ao; kapena tionetseni ife zinthu zimene zilinkudza.

23Yoh. 13.19Tchulani zinthu zimene zilinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, chitani zabwino, kapena chitani zoipa, kuti ife tiopsedwe, ndi kuona pamodzi.

24Taonani, inu muli achabe, ndi ntchito yanu yachabe; wonyansa ali iye amene asankha inu.

25Ndautsa wina wakuchokera kumpoto; ndipo iye wafika wakuchokera potuluka dzuwa, amene atchula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.

26Ndani watchula icho chiyambire, kuti ife tichidziwe? Ndi nthawi zakale, kuti ife tinene, Iye ali wolungama? Inde, palibe wina amene atchula, inde, palibe wina amene asonyeza, inde palibe wina amene amvetsa mau anu.

27Poyamba Ine ndidzati kwa Ziyoni, Taona, taona iwo; ndipo ndidzapereka kwa Yerusalemu wina, amene adza ndi mau abwino.

28Yes. 63.5Ndipo pamene ndayang'ana, palibe munthu; ngakhale mwa iwo, palibe phungu, amene angathe kuyankha mau, pamene ndiwafunsa.

29Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help