Zekariya 13 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Kuyeretsedwa ku Tchimo

1“Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.

2“Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa.

3Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.

4“Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu.

5Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’

6Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’

Kukantha Mʼbusa, Nkhosa Kubalalika

7“Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga,

ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!”

akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Kantha mʼbusa

ndipo nkhosa zidzabalalika,

ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.

8Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse,

“zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka;

koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.

9Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto;

ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva

ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide.

Adzayitana pa dzina langa

ndipo Ine ndidzawayankha;

Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’

ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help