Masalimo 39 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 39Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

1Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga

ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;

ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero

nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”

2Koma pamene ndinali chete

osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino

mavuto anga anachulukirabe.

3Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,

ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;

kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:

4“Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga

ndi chiwerengero cha masiku anga;

mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.

5Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,

kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;

moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.

Sela

6Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:

Iye amangovutika koma popanda phindu;

amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.

7“Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?

Chiyembekezo changa chili mwa Inu.

8Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;

musandisandutse chonyozeka kwa opusa.

9Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga

pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.

10Chotsani mkwapulo wanu pa ine;

ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.

11Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;

mumawononga chuma chawo monga njenjete;

munthu aliyense ali ngati mpweya.

Sela

12“Imvani pemphero langa Inu Yehova,

mverani kulira kwanga kopempha thandizo;

musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,

popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;

monga anachitira makolo anga onse.

13Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala

ndisanafe ndi kuyiwalika.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help